Timba sports alert

Timba sports alert

Share

Sports

03/12/2025

*TNM SUPER LEAGUE* _Log Table Standings:_

02/12/2025

Esau Kanyenda no more!

Sad day! We have lost former Flames striker Esau 'Black Mamba' Kanyenda at the age of 43

May His soul rest in peace ๐Ÿ’”๐Ÿ•Š๏ธ

26/11/2025

Super League of Malawi (Sulom) yavomera kuti yalandira kalata ya madandaulo yomwe Mighty Wanderers yawalembera yokhudza masewero ndi timu ya Silver Strikers.

Wanderers inadandaula kuti oyimbira pamasewerowa, Samuel Fudzulani, anawakanira chigoli chomwe osewera wawo, Clement Nyondo, anagoletsa zomwe kwaiwo akuti panalibe offside ili yonse.

Manoma apemphanso kuti masewerowa awunikidwe ndikuwapatsa mapointi onse atatu kamba koti pachilungamo iwo ndi amene anapambana ngakhale anathera kufanana mphamvu pogoletsana zigoli ziwiri kwa ziwiri.

Timu yaku Lali Luban yatinso oyimbirayu apatsidwe chilango komanso asadzaimbire masewero ali onse a timuyi.

Koma poyankhapo, wachiwiri kwa mlembi wa Sulom, Donnex Chilonga, wati akhala pansi ndikuunika zomwe Manoma adandaula ngati zili zoona kapena ayi kudzera ku National Football Referees Association (NFRA).

Chilonga watinso asanapange ganizo pa nkhaniyi akagogoda khomo la komiti ya oyimbira ku Football Association of Malawi (FAM) ndicholinga choti nawonso ayikepo mlomo pa nkhaniyi.

Manoma ali panambala yachiwiri mu TNM Super League ndimapointi 52 pamasewero 22, pamene FCB Nyasa Big Bullets ndiyomwe ikutsogola ndi mapointi 53 pamasewero 23.

26/11/2025

๐Ÿšจ๐Ÿšจ๐Ÿšซ Globo: โ€œNeymarโ€™s SEASON for 2025 is OVER due to the new KNEE INJURYโ€. โš ๏ธ๐Ÿ‡ง๐Ÿ‡ท

21/11/2025

Mphunzitsi wa timu ya Silver Strikers, Peter Mgangira, wati amailemekeza Mighty Wanderers koma samayiopa akafika pa bwalo la masewero.

Mgangira walankhula izi pamene amafotokoza za m'mene osewera ake akonzekerera masewero a TNM Super League omwe akhale akukumana ndi Wanderers mawa pa bwalo la Bingu mu nzinda wa Lilongwe.

Mphunzitsiyu wati wauza osewera ake zakufunikira kopambana masewerowa kuti atolere maponti onse.

Iye wati tchuti cha masewero chomwe anali nacho kamba ka masewero opimana mphamvu omwe Flames inali nawo zapereka mpata oti akonze malo ena.

Silver ili panambala yachitatu ndi mapointi 40 pamasewero 20, pamene Manoma akutsogola mu ligiyi ndi mapointi 51 pamasewero 21.

21/11/2025

Pali mphekesela yoti osewera otseka kumbuyo wa timu ya Civil Service, Charles Mafaiti akhala akusiya kutumikira timuyi pakutha pa season ino pomwe mgwirizano wake ndi timuyi ukhale ukutha mwezi wa December.

Manong'onong'o akuti timu ya Civil ikuyeseyesa kufuna kuonjezera mlingo wa mgwirizano wa timuyi ndi osewerayu koma izi zikuvuta kamba koti Civil sili yokonzeka kukwanilitsa zomwe Mafaiti akufuna.

Pakumvekanso kuti timu ya Silver Striker ikutsatila mwa chidwi nkhaniyi ndipo ndiyokonzeka kulandira Mafaiti ku banja la Ma Banker Civil Ikaodzera.

19/11/2025

Mphunzitsi wa timu ya mpira wamiyendo ya dziko lino ya Flames, Kalisto Pasuwa, wati sanathe kugwiritsa ntchito osewera monga Uchizi Vunga komanso Andrew Joseph chifukwa amayang'aniranso zotsatira za masewerowo.

Pasuwa wati anali masewero apamwamba amene ngakhale anasintha osewera asanu omwe amayamba-yamba, koma amayang'aniranso chipambano zomwe zinatheka.

Malingana ndi mphunzitsiyu, Vunga ndi Joseph sanathe kuwagwiritsa ntchito kamba koti munthawiyi timu inali ikutsogola, zomwe zikanapereka zoyankhula zochuluka timuyi ikanagonja kapena kuchinyitsa munthawi yomwe iwo alowetsedwa.

Iye walankhula izi atagonjetsa Lesotho 1-0 pamasewero apaubale omwe analipo dzulo pa bwalo la Toyota ku Bloemfontein m'dziko la South Africa.

Mayele Malango ndiamene anagoletsera Flames mumphindi 25 atalandira mpira kuchokera kwa Lloyd Aaron, kutsatira kusewera kwa pamwamba kwa osewera wa kutsogolo Babatunde Adepoju.

18/11/2025

Full Time
Lesotho 0_1 Malawi
Malango 25'

17/11/2025

1978, ๐Ÿ‡ณ๐Ÿ‡ฌ Nigeria did not qualify for the World Cup
1978, ๐Ÿ‡ฆ๐Ÿ‡ท Argentina won the World Cup ๐Ÿ†

1986, ๐Ÿ‡ณ๐Ÿ‡ฌ Nigeria did not qualify for the World Cup
1986, ๐Ÿ‡ฆ๐Ÿ‡ท Argentina won the World Cup ๐Ÿ†

2022, ๐Ÿ‡ณ๐Ÿ‡ฌ Nigeria did not qualify for the World Cup
2022, ๐Ÿ‡ฆ๐Ÿ‡ท Argentina won the World Cup ๐Ÿ†

2025, ๐Ÿ‡ณ๐Ÿ‡ฌ Nigeria did not qualify for the World Cup
2026, ๐Ÿ‡ฆ๐Ÿ‡ท โ“

17/11/2025

Nduna yoona nkhani za masewero, Patricia Wiskes, tsopano yafika ku Soche mu nzinda wa Blantyre komwe kuli bwalo la Mighty Wanderers.

Ntchito yomanga bwaloli ikuyenda bwino zomwe nzosiyana ndi zomwe zili ku Zingwangwa kumene ntchitoyi inayima.

Bwalo la masewero la Zingwagwa ndi la FCB Nyasa Big Bullets.

17/11/2025

๐Ÿšจ๐Ÿšจ Nigeria coach: โ€œDuring penalty session, the guy from Congo did some VODOO. I am SURE OF WHAT I SAWโ€.

17/11/2025

Yesterday's Results

World Cup Qualifiers ๐ŸŒ Europe
๐Ÿ‡ต๐Ÿ‡น Portugal 9-1 Armenia ๐Ÿ‡ฆ๐Ÿ‡ฒ
๐Ÿ‡ญ๐Ÿ‡บ Hungary 2-3 Ireland ๐Ÿ‡ฎ๐Ÿ‡ช
๐Ÿ‡ฆ๐Ÿ‡ฟ Azerbaijan 1-3 France ๐Ÿ‡ซ๐Ÿ‡ท
๐Ÿ‡บ๐Ÿ‡ฆ Ukraine 2-0 Iceland ๐Ÿ‡ฎ๐Ÿ‡ธ
๐Ÿ‡ฆ๐Ÿ‡ฑ Albania 0-2 England ๐Ÿด๓ ง๓ ข๓ ฅ๓ ฎ๓ ง๓ ฟ
๐Ÿ‡ท๐Ÿ‡ธ Serbia 2-1 Latvia ๐Ÿ‡ฑ๐Ÿ‡ป
๐Ÿ‡ฎ๐Ÿ‡ฑ ๐ŸŸฅ Israel 4-1 Moldova ๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ฉ
๐Ÿ‡ฎ๐Ÿ‡น Italy 1-4 Norway ๐Ÿ‡ณ๐Ÿ‡ด

International Friendlies ๐ŸŒ
๐Ÿ‡บ๐Ÿ‡ธ USA 2-1 Paraguay ๐Ÿ‡ต๐Ÿ‡พ
๐Ÿ‡ฌ๐Ÿ‡พ Guyana 2-1 Bonaire ๐Ÿ‡ฎ๐Ÿ‡จ
๐Ÿ‡ซ๐Ÿ‡ท Saint-Martin 0-1 Belize ๐Ÿ‡ง๐Ÿ‡ฟ
๐Ÿ‡จ๐Ÿ‡ด Colombia 2-1 New Zealand ๐Ÿ‡ณ๐Ÿ‡ฟ
๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ฝ Mexico 0-0 Uruguay ๐Ÿ‡บ๐Ÿ‡พ

WSL ๐Ÿด๓ ง๓ ข๓ ฅ๓ ฎ๓ ง๓ ฟ
Aston Villa W 1-3 London City Lioness W
Liverpool W 1-1 Chelsea W
Brighton W 4-1 Leicester City W
West Ham United W 3-1 Everton W
Tottenham Hotspur W 0-0 Arsenal W

Torneo Betano ๐Ÿ‡ฆ๐Ÿ‡ท
San Lorenzo 1-1 Sarmiento Junin
๐ŸŸฅ Independiente 1-0 Rosario Central ๐ŸŸฅ
Velez Sarsfield 0-0 River Plate
Instituto 0-0 Talleres Cordoba

Serie A Betano ๐Ÿ‡ง๐Ÿ‡ท
Santos 1-0 Palmeiras

Serie A Women ๐Ÿ‡ฎ๐Ÿ‡น
SSC Napoli W 1-0 Inter Milan W
AS Roma W 1-0 SS Lazio W
Juventus W 2-0 Genoa W

Emperors Cup ๐Ÿ‡ฏ๐Ÿ‡ต Semi Finals
Machida Zelvia 2-0 FC Tokyo
Vissel Kobe 2-0 Sanfrecce Hiroshima

Liga Portugal 2 ๐Ÿ‡ต๐Ÿ‡น
Feigueiras 1932 1-1 Farense
Leixoes 0-1 Chaves

La Liga 2 ๐Ÿ‡ช๐Ÿ‡ฆ
AD Ceuta 1-2 Leganes
UD Almeria 3-0 Cadiz
Sporting Gijon 1-1 SD Eibar
CD Mirandes 0-2 Burgos CF
Cordoba 1-3 Deportivo La Coruna
Real Zaragoza 1-0 SD Huesca

Serie B Superbet ๐Ÿ‡ง๐Ÿ‡ท
Criciuma 2-0 Botafogo SP
America MG 1-1 Cuiaba
Goias 1-0 Novorizontino
Ferroviaria 1-2 Paranaense

Want your business to be the top-listed Gym/sports Facility in Blantyre?

Click here to claim your Sponsored Listing.

Location

Category

Website

Address

Blantyre