All About Sports

All About Sports

Share

Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from All About Sports, Sport & recreation, Dedza.

08/05/2023

TNM Super league


Week 05
12th May 2023
⚽Bangwe All Stars 🆚 FCB Nyasa Big Bullets


13th May 2023
⚽Silver Strikers 🆚 Mighty Tigers


⚽Moyale Barracks 🆚 Mighty Mukuru Wanderers


⚽Blue Eagles FC 🆚 Dedza Dynamos

⚽Kamuzu Barracks 🆚 Red Lions


⚽Karonga United 🆚 Civil Service United

14th May 2023
⚽Ekwendeni Hammers 🆚 MAFCO FC

⚽Chitipa United FC 🆚 Extreme FC
:2:30pm
.....✍️✍️

06/05/2023



⚽Nyasa Big Bullets 🆚 Moyale Barracks
Stadium

Your Prediction......

04/05/2023



Timu ya Silver Strikers kudzera kwa ma loya ake, yapereka umboni ku bungwe la FAM, owonetsa kuti Hassan Kajoke analandira 3 million Kwacha ngati chipondamthengo (signing-on fee) komanso malipiro a miyezi iwiri (450,000 Kwacha) miyezi ya January ndi February.

Bungwe la FAM linalembera timuyi kuti itulutse umboni oti Kajoke anasayina mgwirizano wa zaka zitatu ndi timuyi, kuyambira pa 04 January, 2023 mpaka 03 January, 2026 ndipo analandira kale ndalama za mgwirizanowu.

Mu kalata yawo, ya pa 28 April, 2023, ma loya a timuyi ati sakukhutira ndi mmene bungwe la FAM likuyendetsera nkhaniyi chifukwa osewerayu samayenera kuloledwa kuseweranso mpira kufikira nkhaniyi ithe mwa chilungamo komanso motsata malamulo.

Timu ya Silver, kudzera kwa ma loyawa, yati ndi yodabwa kuti Kajoke anasewera nawo masewero a ligi amene timu ya FCB Nyasa Big Bullets inasewera ndi Extreme FC pa 29th April, 2023 ku Lilongwe.

Timu ya Silver inakasuma ku bungwe la FAM kuti lipatse Kajoke chilango chosaseweranso mpira kamba ka ukamberembere ndi chinyengo pamene anasayinanso mgwirizano wa zaka zitatu ndi timu ya Nyasa Big Bullets chonsecho anasayina kale mgwirizano wina ndi timu ya Silver.

......✍️✍️

04/05/2023

wadandaula.....

Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers Pieter De Jongh waloza chala bungwe loyendetsa masewero a Mpira wamiyendo dziko lino kuti akulephera kuyendetsa bwino masewerowa polola Hassan Kajoke kuti azisewera kutimu ya FCB Nyasa Big Bullets nkhani zake zisanakambidwe.

De Jongh walankhula izi kwa olemba nkhani pam'mene ankonzekera pamasewero awo a mu TNM Super league omwe akhale akusewera ndi Ekwendeni Hammers lamulungu likudzali.

Malinga ndi mphunzitsiyu, Iye wati Kajoke samayenera kumasewera ku Bullets kufikira nkhani zokhuza contract yomwe anasaina ku Silver zitakambidwa.

Mphuzitsiyu wati ngodabwa kuti osewera yemwe board inawuza kuti akubwera anasintha chiganizo ndikusaina gwirizano wina ndi Bullets.

Big Man walira chokweza.....

......✍✍

04/05/2023

Ochemera Bullets ndi Wanderers anena kuti sali okondwa

A Storne Mwamadi komanso a Denis chitsulo , omwe ndi atsogoleri amasapota a matimu a FCB Nyasa Big Bullets ndi Mighty Mukuru wanderers ati ndiosakondwa ndi ganizo la, Boma komanso, Football Association Of Malawi ( FAM ) loimitsa bwalo la kamuzu kuseweredwerapo masewero akulu-akulu kuphatikizapo masewero a Blantyre Derby.

Izi zadza kutsatira kulengeza kwa Bungwe la Football Association Of Malawi, kuti bwalo la kamuzu stadium siloyeneraso kuchititsa masewero akulu-akulu kuphatikizapo masewero a Blantyre Derby, ndipo m'malo mwake masewero a Blantyre Derby pakati pa matimu a Mighty Mukuru wanderers ndi FCB Nyasa Big Bullets adziseweredwa mu mzinda wa Lilongwe pa bwalo la Bingu stadium.

Malingana ndi a Mwamadi, ati Boma likanakomza bwaloli msanga malo omwe ali oonengakawo chifukwa kutengera masewero a Blantyre Derby mu mzinda wa Lilongwe ziphinja masapota ambiri otsatira matimu-wa amchigawo chakumwera.

" Ndikale lomwe tinayamba kudandaula za bwaloli ,so akanatikomzera msanga. Monga mukudziwa matimu amapereka ma percent a ndalama akamagwiritsa ntchito bwaloli so atha kutenga ndalama zimenezo ndikukomza malo omwe salibwinowo. Tipepha Boma litiganizire chifukwa apa tikhala kuti tapha ochemera amatimu awiri-wa omwe ali m'chigawo chakumwera kuno omwe sangamakwanitse kupita mu mzinda wa lilongwe". Iwo atero.

Pothirapo ndemanga a Dennis chitsulo, omwe ndi mtsogoleri masapota a Mighty Mukuru wanderers wagwiriza ndi mawu a storne Mwamadi kuti Boma komanso Football Association Of Malawi,kuti likhanzikitse ndondomeko yabwino yokomza malo omwe ali oonengeka pa bwalo li.

" Nkhani imeneyi ife tailandira koma ndizodandaulitsa Blantyre Derby kumakamenyera ku Lilongwe koma tingopepha Boma kuti litithandize msanga . Ndim'mene kwacha ikuyendera pano sindikukhulupilira kuti ambiri adzikwanitsa kulondora timu mu mzinda wa lilongwe. A chitsulo anatero.

....✍️✍️
Zampira sakwiya!

Want your business to be the top-listed Gym/sports Facility in Dedza?

Click here to claim your Sponsored Listing.

Location

Telephone

Website

Address

Dedza