Lobi Young Soccer FC

Lobi Young Soccer FC

Share

Lobi Young Soccer FC is a Football Club from Lobi Trading Center in Dedza District , currently playing in League Two of Central Region Football Associations.

12/07/2026

Big shout out to my newest top fans! McDonald Mwase, Chipie Chicharito Kasamba, Hâzwël Hãdzëy Mbïrïyãkùlā Dzüwã, Blessings Nkhoma, Mandevu Vanancio, Peter Chitowe, Kelvin Crifton Salimon

05/07/2026

VOTE OF THANKS (KUTHOKOZA)
Ine monga admin wanu yemwe pano ndi kupuma Kaye chifukwa choti ndatalikira ndi Kwa Lobi ndati ndikuthokozeni kuti Tayenda bwino ZEDI, ndipo inu ndi athu abwino.

Mwina kutheka Tsiku Lina tinalemba zosakusangalasani inuo mungoziwa kuti moyo ndi choncho basi sitingasangalase aliense.

Pamwamba pa Zonse tiyeni tiziwe kuti Social media ili ndi mphavu yopitisa uthenga pomwe ife sitingafikire tiyeni tipitilize kupanga follow and share this page kuti page yathu ikule.

Chomaliza tinatulusa advert yoti tufuna muthu oti azitipangira manage page yathuyi, timuthokoze muthu yemwe azipereka kuti azipanga manage page yathuyi ndipo ndi muthu yekhayo yemwe anatumiza Email yosonyeza kuti akufunadi kumapanga manage this page (Enao a nalephera kutumiza Email "Kaya matumizidwe a Email zimawapeta Kaya, kapena unali moto wa mapesi aziyankha okha") LET'S WELCOME OUR NEW ADMIN ALL THE BEST

04/07/2026

Announcement/zolengeza
Pa Monday ndi Tuesday likubwerali thawi ya 9:00AM tikhala tikupangitsa ma trials pa Lobi Community Ground pa ma position onse 11 kuyambira pa gole, madifenda, ma Midi ndi ma sitirayika.
Zofunikira kwa player yemwe akufuna kuzayetsa mwayiwu
1. Ubweretse chiphatso cha unzika(National ID)
2. Ukhale wa zaka 23 kusika pansi (izi tukamba zaka zaku mpira paja "u get me")
3. Zipangizo zomenyera mpira ngati ma BUTI mukuyenera kubweretsa zanu(wa beyaa ayi iwe nde usayerekeze kubwera)

AUZENI AZANU, A BRO, A NEBA NGATI KWAWO KULI MWANA WA LUSO ABWERE MWINA ULENDO WAKE WOKAMENYA SUPER LEAGUE ULI KWA LOBI.

Thwawi ino tupereka mpata kwa ma coach apa social media /online paja Ena tinayamba kale kuti ku team zambiri zikufunika kukonzedwa thawi yanu ndi iyi pezani ma player omwe mukuwaganizira ndipo abwere pa Ground ma ASSESOR azawaone timange Team ya phamvu chifukwa la Tuesday ndi Tsiku lomaliza kulembetsa ma player omwe atatumikire CRFA LEAGUE TWO YA 2026 /2027 SEASON, Ziwani kuti league tikumenyayi ndi ya professional akaseka transfer window amakhala kuti aseka palibe zoti tikatenga player wa kwa Chinkhu kutithandizira ayi ayi mwachidule ngati sunapangitse Card kuzera mu ndondomeko ya CRFA sungamenye nao league kufikira azaseguletso Transfer window.

Kaya massage yatalika Koma ndangofuna tiunikirane kuti zimakhala motani kutengera experience yomwe tinayipeza ku Ma online coaches

Zikomo kwajinji

30/06/2026

Thanks alot kwa omwe mwatengapo mbali Mawa tibweretsa List

30/06/2026

Today's Facts(Team ndi yathu)
1.Team ndi yathu (Awa ndi mawu omwe ambiri timakonda kuwagwiritsa Ntchito) Team yavutika kupeza Registration Fee athu omwe mumaoneka ngati oyikonda mwalephera kuyithandiza (Kodi Tikamati team ndi yathu ndipo timayikonda Love yake iti)
2. Athu Ena akabwera kuti athandize team zoyakhula kuchuluka nomwenu mu kulephera kusokha or k500 or K1000 Sikuti ndilamayo mulibe (Team ndi yathu iyi timayikonda)
3. Inu mumati team ndi yathu koma mu kulephera kuchitapo kathu Chaka Chino cha 2026/2027 Mukhale ochita ngati oyikonda ndipo ngati mu kuziwa kuti simuzichitapo kathu ndibwino museke pa kamwa.

Team ndi yathu, Tinayivutikira, ndiyakwathu Mawu awa ndi a Chabe ngati simukupanga action iriyonse pothandiza team.

Wina avekele ine ndimathandiza poichemerela team basi if your not doing any action iweo usanduka wa ganyu.

Tithokoze anthu onse omwe mwasokha /we can officially Comfirm That Lobi Young Soccer FC imenya League this Season.

27/06/2026

To: Lobi Community football lovers
Monga lero ndi Tsiku lomaliza komanso potengera ndimomwe tikuperekera zikuoneka zovuta zedi unless a miracle happens. By close of business today tipereka report kuti tayesesa motani kumbali yathu ndipo zikakhala kuti zativuta Atleast pasakhale wina woloza chala mzake pa decision yomwe ingasatile Chifukwa tonse tinapasidwa mpata oti Tichitepo kathu.

Zikomo

25/06/2026

Ziwani izi ndipo chitaniponi kathu athu akwa Lobi
Tithokoze Zefaniya Anderson potumiza K5000
Muziwa zoti athu pa gulu pano tilipo 1300 atati wina aliense mwina wachitapo action Kaya ku pereka K2000 or K1000 or K500 Muziwa zoti titha kupeza ndalama yoposera 1 Million tisagwe mpwayi kuti aaaaa ka ndilama aka kachepa inuo tangotumiza tikamphatikiza ikhala ya mbiri paja tasala ndi masiku Awiri.

"Ukawerenga message iyi chitapo kathu "

24/06/2026

So far zero contribution 4days to go
(kufika panopa palibe wapelekako)

23/06/2026

5 days to Go a Sis a Bro mukadaganizabe Tivungileni mulinako (Ngati sitikuponya kangachepe tilinako ndekuti tiyiwale loto lowonera mipira pa Lobi Community Ground)
Ndipo Chaka Chino kuli Zikho zitatu ( League Two, National Bank Cup and Chipiku stores Cup)

Want your business to be the top-listed Gym/sports Facility in Dedza?

Click here to claim your Sponsored Listing.

Location

Category

Website

Address

P. 0 Box 45/Dedza/Lobi Trading Center
Dedza