08/08/2023
It's on already
Transfer news
Timu ya silver strikers ili ndi mwayi okhalabe ndi chimwemwe idana ngakhale atapanda kumuguliratu izi zili chonchi kamba koti timu ya mbeya yati itha kumusiya katswiliyu kwa myezi ina isanu ndi umozi ngati njila imozi yowapasa mpata a silver k*t aganize bwino pa za offer ya nkuluyi
Clement nyondo wa dedza dynamos ndi osewela ekhayo emwe akufunidwa ndi ma timu otchuluka dziko muno nyondo Ali pa list ya ma timu monga nyasa BB mukuru wanderers ingakhaleso silver strikers nthawi yake yokhala ku dedza ukuoneka ngati ikupita kumapeto
Nayo timu ya mighty mukuru wanderers yalengeza k*ti yatengaso osewela wao wakale Francisco madinga Ndipo nkuluyu wa tikitila zaka ziwili ku lali luban
Calisto pasuwa wati akufuna anyamata ake ena omwe anawabwelekesa kuma timu ena k*ti abwele chigao chachiwili cha ligi awa ndi anyamata monga mphatso magareta ku ekwenden hamers komaso anyamata awili Ali ku bangwe mlongen ndi Salima..
Za brighton munthali nde munanva kale
Nayo chitipa yati sikugulitsa player aliyese malo mwake ikufuna kuonjezela moto ndi osewela waku tsogolo ku Tn Star China Chirwa
Bye bye for now
✍️Sabufa uja
26/07/2023
Dragon fc imatha ku sewela mu stadium yopanda ma sapota ndik*tenga chikho 🤔 ofunika kusamala apapa
26/07/2023
Nyambose amuchokochaso
Patatha ma siku awili timu ya bangwe all star chilengezeleni kubudulidwa kwa aziphunzitsi ake awili. Tithaso kukusimikizilani k*ti nayo timu ya mighty waka waka tigers yabandula mphunzitsi wao wankulu omwe Ali a Christopher Nyambose kamba ka kusachita bwino muma sewela ake okwana asano mu tnm superleague komaso k*tulusidwa mu FDH cup ndi timu ya Nsanthe admarc
Ndipo malo mwake wachiwili kwa mphunzitsiyu emwe Ali Robert Baggio n'gambi ndiamene wagwilizila ntchito yau mphunzitsi ku timuyi,,,,
Anaona sadabwa
✍️Sabufa uja
19/04/2023
Kuthyola khobwe ndi m'mawa
Sabata yachiwili otaya ak*taya ndipo otola ak*tola
Northern battle time ya Karonga united yaitana anyamata a chitipa pa karonga stadium lomwe Lili loweluka likubwelali
Nawo asilikali a redlions amene anakatenga point imozi ku Lilongwe Ali pakwao pa Baraka k*thamangitsana ndi anyamata a Mighty mukuru wanderers...
Nkhondo ikupitilila loweluka lomwelo pomwe ma central region giants akhale akukumana ku area 30 nankhaka ground anyamata azipewa za phala atengetsana chulu cha Chula ndi ma central bankers a de Jong
Nayo bangwe all star yomwe yayamba mosakhumudwitsa ikhala ili pa chiwembe k*thambitsana ndi Ana akumpanda Waka Waka tigers ..kodi mulowela k*ti pa tsikuli?
Tnm superleague izakhala ikupitilila Sunday pomwe civo sporting yomwe inayenda ulele ku mwela yaitanitsa extreme fc
Nayo ikwendeni izakhala ili pakala Pukalani ndi asilikali akukaning'ina moyale barracks ..FCB Nyasa bullets ikufuna itabweza chipongwe chomwe inalandila pa Dedza stadium chaka Chatha pomwe yaitanitsa asilikali aku salima Mafco ku kamuzu stadium
Nayo timu ya Dedza dynamos izakhala ili pakwao ndi asilikali aku Lilongwe kamuzu barracks
Ulipo wa HARRISON DE JONG PASUWA NDI KANANJI
BYE BYE FOR NOW
like n share
15/04/2023
Wa Lero si wamasewela
Ma bankers available
Awa
14/04/2023
Wadya nganga wadya nkhuku
inu mulowela k*ti
23/03/2022
WACHIONA NDANI..
Timu ya malawi yomwe anyamata ake ndiosachepela zaka zakubadwa 23 tsopano ili mu dziko la turkey komwe ikuimbekeza kusewela ma sewelo awili mu ndime yachipulula ndi ma timu a kuwait komaso togo junior flame yapita ndi patrick mabedi decreck nsakakuona komaso mario marinica ngati mphunzitsi wankulu
Nanga TNM SUPERLEAGUE yatibwelesela zotani ku mapeto a sabatayi
Ma timu akhala ak*thamangitsana ndicholinga chofuna 3 points k*ti athe kulimbitsa mwai ofuna kukhala akatswili a league.. paja amati k*thyola khobwe ndi mmawa liwilo lapancjenga timayambila limodzi Silver strikers yomwe inaona zakuda sabata langothali ku balaka yaitanitsa anyamata a Rumphi united omweso zao sizinayambe bwino kweni kweni kusatila ndi kugonja pakhomo ndi Dedza dynamos
Mighty wanderers yomweso ikuchokel a kuchilango chongothamanga ulele chomwe inapasidwa pa kamuzu stadium sabata yatha yaitana TN stars yaku kasungu yomweso ikuchokela kososoledwa ngati nkhuku ndi timu ya Ekwendeni ndipo masewela Amenewa akachitikila pa chiwembe
Redlions yomwe inakantha mwankhaza silver strikers ikhala ikugwilitsaso nchito mwai osewela pakhomo pomwe ilandile alendo ochoka ku karonga a karonga united pa balaka stadium
Moyale barracks masoja omwe anaonesedwa zakuda ndi ana akumpanda sabata lapitali akhala ali pakwao k*thambitsana ndi anyamata a m'boma a civo servis united omwe akuchoka k*tapa 3 points yose pamwamba pa timu ya sable
SUNDAY JOUNEY CONTINUE otola ak*tola ndipo otayao ndizao ...
Dedza dynamos yomwe ikuchokela chigao chakumpoto komwe ku rumphi kumene inakasokoneza ndikuba ma poits ose atatu pa bwalo la rumphi yaitana anyamata aku mpoto komweko a karonga united k*ti azaonesane chamuna pa balaka stdium
Nayo Ekwenden hammers igwilitsa ntchito mwayi osewela pakhomo kachikena pomwe ikhale ikupindilana ndevu mkamwa ndi asilikali aku salima a mafoco omweso zao sizinayambe bwino
Sable farming ma sable akhala ali pa home ndi timu ya tigers yose ikuchoka k*tibula ma soja a moyale
#
21/03/2022
TNM SUPER LEAGUE
Ma timu tsopano ayamba ntchito yotolela ndi k*taya ma points mu league yaikulu dziko muno..
Nkhondo ya angitawo inayamba pa kamuzu stadium pomwe ma Defending champion a nyasa big bullets akwapula monvesa chisoni anyamata a mighty wanderers ndi zigoli ziwili kwa chimozi
Nayo timu ya ekwendeni hamers yagwilitsa ntchito mwayi osewelela pakwao pomwe yatibula anyamata a ku kasungu TN stars ndi zigoli ziwili kwa chilowele
Karonga united yomwe masophenya ake ndi k*tenga superleague chaka chino motsogozedwa ndi magaya sinayambe bwino maloto ake pomwe yalandila chaulele chodzadza ngakhale inali pakhomo koma asilikali aku lilongwe anaononga chitetezo chose chaku karonga pomwe anaibatiza ndi zigili zokwana zitatu kwa chimozi
Nkhondo sinathele pomwepo ...anyamata anapitiliza k*tulusana thuk*ta ndi ukweche lamulungu pomwe timu ya silver strikers yachoka chizolika pa balaka stadium itasiya ma points ose atatu ndikubwelela opanda kalikose ku lilongwe pomwe anyamata a redlions anagwilitsa ntchito mwayi osewelela pakwao pogagada ma banker ndi chigoli chimozi kwa zii
Nayo timu ya tigers yatibula mwankhaza asilikali aku kaning'ina a moyale ndi chigoli chimozi kwa chilowele
Rumphi united yagwila fuwa lamuto pomwe yapalidwa mamba pakhomo ndi zigoli ziwili kwa chilowele ndi alendo anzao a Dedza dynamos
Nao anyamata a civo akwapula ndikupha mwankhaza katswili a sable farming powabatiza ndi zigoli ziwili kwa iyayi
Asilikali a mafco achitaya okha pakwao pomwe apambazidwa chigoli chimozi kwa chilowele ndi apolice aku area 30 blue eagleas
TNM SUPER LEAGUE WEEK 1 RESULTS
Nyasa big bullets 2 1 mighty wanderers
Ekwenden hammers 2 0 TN stars
Karonga united 1 3 KB
SUNDAY ⚽️⚽️
Redlions 1 0 silver strikers
Civo 2 0 sable farming
Rumphi 0 2 Dedza dynamos
Mafco 0 1 blue eagles
Tigers 1 0 moyale
Wadya nganga wadya nkhuku
✏