01/02/2025
ZATHAPO!
Stanly Biliat watsazika ku nyasa big bullets kutsatira kutha kwa contract yake ndipo anakana kusaina contract ina ndi bullets Ndipo mphekesera zikumveka kuti akhale akulowera ku EKHAYA FC kutsatira ENOS CHATAMA
31/01/2025
Transfer News!!
Forward Christopher Gototo is set to join newly promoted Super League of Malawi side, Ekhaya FC on loan from Silver Strikers FC .
The former Ascent Academy and Blue Eagles FC striker played for Civil Service United FC on loan last season.
It is understood that the player wanted to terminate his contract with the bankers due to lack of game time but his request has been denied.
31/01/2025
Civil yalola Masiya Manda kugula kontirakiti
Timu ya Civil Service United yavomera chiganizo chomwe osewera kumbuyo mu timuyi, Masiya Manda, wapempha kuti agule kontirakiti yake pa mtengo wa K10 million.
Izi ndimalinga ndi chikalata chomwe Civil yalemba kutsatira pempho lomwe m'khalapakati wa osewerayu, Robert Ng'ambi, analembera timuyi.
Osewerayu analembera Football Association of Malawi (FAM) kuti ilowelere pa pempho lake zomwe bungweli linakana kuti chofunikira nchoti mbali ziwirizi zimvane ngati ana amodzi.
Mkulu wa timuyi, Edgar Chipalanjira, wati wavomera pempholi ataunika bwino lomwe za nkhaniyi.
Chipalanjira wapempha m'khalapakati wa osewerayu kuti atumize ndalamayi mwansanga ndicholinga choti apeze osewera wina oti alowe m'malo mwake.
30/01/2025
Congratulate Mr. Eliya Guardiola Kananji who has signed a 2-year contract with the team as head coach.
Congratulations coach!
30/01/2025
Calisto pasuwa ndi mphunzitsi wa flames
26/10/2024
𝐌𝐀𝐓𝐂𝐇 𝐃𝐀𝐘 ⚽
🆚 Mighty Mukuru Wanderers
🗓️ 26 October | 15:00
🏟️ Kamuzu Stadium
🏆 TNM Super League
#️⃣
09/09/2024
Dedza ikuyenera kupisa m'thumba kuti ipereke K10 million, pamene Wanderers ilipira K4 million pa nkhani ya Kamwendo.
Osewerayi abwelere kaye ku Dedza komwe amalizitse kontirakiti yosala.
Football Association of Malawi (FAM) kudzera ku komiti yomwe imaunika nkhani yokhudza osewera kutsogolo, Promise Kamwendo, yagamula timu ya Premier Bet Dedza Dynamos kuti ibweze ndalama zokwana K3 million komanso K4 million zomwe inalandira kuchokera ku matimu a FCB Nyasa Big Bullets komanso Mighty Mukuru Wanderers.
Izi zikudza kutsatira kuunika kwakuya kwa nkhani ya osewerayu yemwe anasainira mgwirizano wa zaka zitatu ndi Manoma ngakhale amayenera ku lowera ku Mapale potengera kuti anali atalipira kale ndalama za osewerayu.
Komitiyi yalamulanso kuti Kamwendo abweze ndalama zokwana K6 million zomwe analandira ku Lali Luban paza m'gwirizano wawo kamba ka kontirakiti yomwe anasainira.
Mighty Mukuru Wanderers ayipeza yolakwa ndipo yauzidwa kuti ilipire ndalama zokwana K4 million kamba ka madulira pa nkhani yokhudza kusaina osewera.
Malingana ndi chigamulochi, Dedza ailipiritsa ndalama zokwana K3 million kamba kofuna kudya mbali zonse ziwiri zomwe ndi zolakwika pa ndondomeko yofuna kugulitsa osewera.
FAM yalamulanso kuti osewerayu abwelere ndikukayambiranso kutumikira timu ya Dedza potengera kuti yathetsa mgwirizano omwe anasainira ndi Manoma.
Komitiyi yapereka masiku atatu kumbali zokhudzidwa pa chigamulo chi kuti zidandaule ngati sizikukhutira pa zomwe zatulukazi.
07/09/2024
Shout out to my newest followers! Excited to have you onboard! Bon Volly, Encok Leisure