29/05/2026
Katswiri wakale wa team ya Mighty Wanderers FC Lawrence Chaziya yemwe pakadali pano akutumikira team ya Simba Bhola mdziko la Zimbabwe Ali pa mndandanda wa Osewera 8 omwe sapezeka nawo mmasewero akubwelawa.
Lawrence Chaziya ali ndima Yellow card awiri ndipo iye pamalamulo sakuyenera kupezeka mmasewero amodzi amu league, timu ya Simba Bhola FC yomwe ili pa number 8 ndi mapointi 20 pamasewero 14 amu league ndipo ikhale ikukumana ndi team ya Triangle FC yomwe ili pa number 17 ndipo ili ndi 8 points pamasewero 14 yomwe nayo yasewera.
Chaziya wakhala osewera odalilika ku team ya Simba Bhola FC season ino ndipo masabata apitawo a apezeka nawo mu team of the week ya mdzikolo pamodzi ndi Binwell Katinji yemwe akutumikira team ya Chicken Inn.
✍️ Obanda 50
DRYBORNE SPORT
29/05/2026
Kieran Ngwenya uja tabesa, waitanidwa kulowa mu camp ya Trinidad & Tobago...
29/05/2026
EASTERN REGION FOOTBALL ASSOCIATION YAIMITSA KUKHAZIKITSIDWA KWA DURATA REGIONAL DIVISION LEAGUE CHIFUKWA CHA MSONKHANO WA NDALE.
Bungwe loyendetsa masewero mchigawo chakummawa la Eastern Region Football Association (ERFA) laimitsa mwambo wokhazikitsa ligi ya Durata Regional Division League One pambuyo poti chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) chakoza msonkhano wandale ku Ntaja, Machinga pa tsikulo ndi nthawi yomweyo.
Malinga ndi kalata yomwe yasainidwa ndi Mlembi Wamkulu wa ERFA, Elia Nyirongo, mwambowu womwe unkakonzedwa pa 31 May 2026 ku Vision Stadium tsopano uchitika pa 6 June 2026.
ERFA yati chiganizochi chakozedwa pambuyo pokambirana ndi okhudzidwa osiyanasiyana atadziwa kuti DPP ichitira msonkhano wake pa bwalo la Michongwe Primary School m’dera lomwelo.
Bungweli lati kuimitsa mwambowu cholinga chake ndi kuonetsetsa kuti kukhazikitsidwa kwa mpikisanowu kukuyenda bwino komanso mwadongosolo.
Ngakhale tsiku lasinthidwa, ERFA yatsimikizira kuti malo ochitira komanso masewera omwe akukonzedwa pakati pa Ntaja Rangers ndi Nselema United sizisintha.
ERFA yapepesa chifukwa cha zovuta zilizonse zomwe zayambitsidwa ndi kusinthaku.
✍️ Calvin Lawrence
DRYBORNE SPORT
28/05/2026
📌Castol Kayuni 10 # might be the next Francisco Madinga, Karonga United Football Club has too much talent in the squad trust me Second round matimu akuluakulu akanganilana.
✍️ Obanda 50
DRYBORNE SPORT
28/05/2026
Wina walemba izi Mchingelezi ku inbox ndipo sakuona vuto ndi mndandanda wa Osewera omwe Pasuwa watulutsa.
Some of the reasons behind Pasuwa’s newly released squad could be the inclusion of many young and foreign-based players, suggesting that the technical panel is using the Ethiopia friendlies to experiment and assess the depth of the team.
Other factors may include players’ current form and fitness, the tactical approach for the Ethiopia friendlies, team balance and chemistry, as well as the desire to test new players ahead of future competitions.
Maganizo anu ndiotani ndipo Kodi mukugwilizana nazo ?
DRYBORNE SPORT
28/05/2026
Zathapo pakati pa Gilbert Chirwa ndi FCB Nyasa Big Bullets Kutsatira mkumano omwe unachitika ndipo agwilizana kuti mphuzitsiyu asapitilize ntchitoyi.
DRYBORNE SPORT
28/05/2026
A Mtedza Chimwemwe Gatuso Idana dziko lakusowani, ena akufunsa kuti kodi nkhani zanu zili pati ku National team, olo ka friendly ngati aka akanatha kudzaukwela.
DRYBORNE SPORT
28/05/2026
Malingana ndi Squad yomwe watulutsa Calisto Pasuwa yama Friendlies ife we are very much OK Inu maganizo anu ndiotani, Kuyamba ndi kutsogolo.
1. Babatunde Adepoju — Venda Academy
2. Christopher Kumwembe — Green Buffaloes
3. Ephraim Kondowe — FCB Nyasa Big Bullets
4. WiseDinho Mpinganjira — Black Bulls
5. Gaddie Chirwa — Mighty Wanderers
6. Chifundo Mphasi — Power Dynamos
7. Robert Saizi — Zanaco
8. Luciano Rundles — Kalonji Soccer Academy
DRYBORNE SPORT
28/05/2026
Flames Final Squad for Ethiopia Friendlies.
Anu alipo angati apa musakhale ngati simukuona.
DRYBORNE SPORT
28/05/2026
Basitu league kungoyamba dzulo nayo Mighty yaonjezera sapota mmodzi Former, Central Region Supporters GS Wilfred Kabwele akhale akulowa mmbanja pa 5 July 2026, kulengeza koyamba ndi uku kupangila omwe sanadyeko ndalama za bwana Mpinganjira kokadyera ndikumeneku.
Thokozani wapata Shuwa apa sizatelemu azingolowa kumpira ulele ndi onse akumudzi kwawo 😂.
CONGRATULATIONS!!
DRYBORNE SPORT