REST IN PEACE LEGEND
Kanyenda
Chinsapo United Football Club
Chinsapo United Football Club is a team from Chinsapo community of T/A Nsewa in the capital city of
Hello coaches,
I need under 14 teams information, only those who are well organized and sustainable teams, only in lilongwe.
Give me the following details in my inbox,
1: Team name
2: head coach
3: qualification of the coach
4: Location of the team
Note: strictly under 14
Please send the massage to those who are not on the WhatsApp forum.
Thank you,
Patrick Kaputa GS for
Lilongwe football coaches association
28/04/2023
Proud of guys!
12/03/2023
Please guys uwu ndimwayi wanu yambani ulendo waukochi, nthawi muli nayonso yochuluka m***a kuyambako kuponya pang,onopangono, yesesani Coaches. Munthawi yanga ngati Chair ndikufuna ma coach ochuluka akhale ndi ma Certificate aukochi kuti aphunzire kuti ukochi ndi chani, apa palibe kunamizira kuti aaaa iyayi ndinamva mochedwa,nthawi yochuluka mulinayo pepani guys ndapota nanu Course mumaifuna ija ndiimeneyi.Tiyeni tikapeza olo kunditumizira ndikakuyikirani ngati mulibe nthawi yobwelera ntauni chonde chonde guys lets do it uwu ndi mwayi wathu.
Uthenga wu waza Course uponyeni Pena paliponse kuti Coach aliyense umufikire pasakhale kunamizira chilichonse.Tsiku lopambana.
Zikomo,
The Chairman
Lilongwe District Football Coaches Association
Coach Gondwe.
18/02/2023
MEETING OF ALL ZONES OF LILONGWE DISTRICT FOOTBALL COACHES ASSOCIATION AT LILONGWE COMMUNITY GROUND ON 18TH FEBRUARY, 2023
-Opening prayer by Likuni-Chinsapo Zone.
PRESENT
1. Nanthenje Zone
2. Mitundu Zone
3. Area 36 zone
4. Likuni-Chinsapo zone
5. Lilongwe District Coaches Committee
6. Kabudula Zone
7. Area 49 Zone
*AGENDAS:*
*1. Zomwe zachitika mma Zone mu chaka cha 2022:*
*Likuni-Chinsapo zone: Committee sili active and palibepo icho yachitapo.
*Mitundu Zone: Committee pachiyambi inali active koma pano yazilara.
*Area 36 Zone: Committe yawoso ndiyakufa.
*Mma Zone ambiri zikuonesa kuti mwakhala muli chetechete makamaka mu chaka cha 2022.
*LDCC chaka cha 2022 yayendera ma zone ngati: Nsalu, Chilinde, Area 49, Biwi, Mitundu, Likuni-Chinsapo, Kabudula.
*LDCC yinatsegula account ku FDH Bank ndicholinga choti kuti ikamapangisa ma course a Coaching anthu azitha kumaponya kumeneko ndalama yopangitsira course yo. Ndipo a Chairman atumiza account number yo pamaGroup onse amaZone a LDCC.
*2. Zomwe zichitike mcha cha 2023:*
-MaCoaches ambiri mmaZone akufunisisa kuti pachiyambi penipeni kuti ma Committee akhale active akuyenera a LDCC apangise mamphunziro a Coaches mma zone.
-Maganizo ena akuti mamphunziro a Coaches akuyenera kuchitika koma kwapanopa kwa ma Leaders a mma Zone kaye.
-Course ya FAM D License 🪪 yonse imakwana K3,000,000 pa anthu 30 koma paliso kuthekera kuonjezerekapo anthu.
-A Chairman a LDCC akhala pansi ndi a FAM kuwapempha kuti mamphunziro a Coaches achitike makamaka a FAM D LICENSE pa anthu ambiri and also pamtengo woti aliyense mkuthekera kupanga nawo ndipo alengeza posachedwapo zomwe iwo ayankhidwa or zomwe apeza. Pamene akhaleso akusaka sponsorship pa mamphunzirowa.
*AOB*
-A Chairman a LDCC ati pomatha chaka chino cha 2023 mamumphunziro a Coaching Course akhalapo ndithu.
-FAM chaka chino yatikonzera ma courses angapo makamaka pa Coaching License ya CAF C mu chaka chino cha 2023 kwa ma Coaches omwe ali ndi FAM D and FAM C License.
-MaDate ake ali motere: mu April kuli course ina, mu June-July kuliso course yina ndi mu September course ina pa mamphunziro Coaching License ya FAM C.
*Ndipo oyenera kukakhala nawo pa CAF C Coaching course iyi akhale mamembala wa Football Coaches Association of Malawi palilipira:
K7500 kwa iwo a FAM D and FAM C
K10000 kwa iwo ali ndi FAM B
K15000 kwa iwo ali ndi FAM A
-Closing prayer by Likuni-Chinsapo Zone
Click here to claim your Sponsored Listing.
Location
Category
Contact the business
Telephone
Website
Address
Chinsapo 2
Lilongwe