09/06/2026
🚨 | BREAKING: Ntaja United have officially parted ways with Mabvuto Tigana Lungu as their head coach.🔚
Chimango Blackberry Kayira,the club's assistant, has been appointed as acting head coach of Ntaja United Football Club with immediate effect.
08/06/2026
Ndayambano kumvela chisoni Ethiopia ija. 🫢
Inu Flames yakonzeka kwambiri kufuna kuzepula Ethiopia mosaimvela chisoni mawa.
08/06/2026
SITINGAMENYE MPIRA ULERE— The Thofaz
Zokonzekera za timu ya Luanar Mitundu Baptist FC yomwe yangolowa kumene mu ligi yaikulu, zabwelera pambuyo kamba Koti osewera atimuyi anyinyilika ndipo akana kuchita ma practices chifukwa kufikira lero lino ndalama zawo za Malipilo sizikulowabe.
Mitundu Baptist, The Thofaz, ilipa nambala 10 pa mndandanda wa momwe aimira matimu 16 mu ligi ndi mapointi asanu ndi awiri (7 points) itakwanitsa kupeza chipambano kawiri, kufananitsa mphamvu pamodzi komanso kugonja katatu pa masewero asanu ndi amodzi omwe yasewera.
______________________________________________
Like and follow Mpira Online
08/06/2026
DANGER WAPAKIRA KU TIMES WALOWERA KU JOJO FM
Williams Gondwa, yemwe amadziwika ndi dzina loti Danger Left Winger, wasintha nthabwa pomwe wachoka Times Radio mkuyamba ntchito ku JOJO FM malingana ndi zomwe yalemba wailesi ya Jojo mamawa uno pa tsamba lake la mchezo la Facebook.
“Tithandizeni kulandira katswiri oulutsa nkhani za masewero Williams Gondwa amene amadziwikanso kuti Danger Left Winger pamene wapanga join team ya nkhumekume zoulutsa mawu pa wayilesi ya JoJo 100.4 komanso 100.6 FM.”
_____________________________________________
🗣️🎙️ Open fayaaaaaaaaaaaaaaaaaaa! Kudzaphonya chikadakhala chigoli, mwayiiiiiiiii goalkeeper mbambande anasiya nthaka ndikumata Mpira ngati mmanja muli ulimbo... Mzanga Isaac Salimaaaa! Khuda Muyaba anazula buleti la mphamvu kwambiri bwezi tikukamba kuti ndi momujabe 0-0. 🙌😅
🗣️🎙️ Yes, referee waliza pinto yake Akuti panali ngati kukankhana-kankhana ndiye ndi Mpira wapansi. Kudzangowutsetseletsa wamphamvu kwambiri ngati madzi ayamba mafunde pa Nyanja, apite Emmanuel Savieli kubwiza njomba yoyamba yachiwiri mkudzatheka, kudzakokotela-kokotela kumene kuja koma Peter Cholopi waima njiii ngati chitsa chotsala mulupsya 🙌😅
🗣️🎙️ YEEESSSSSS, grade 1 referee Godfrey Nkhakananga waliza pinto, kuti chigawo chachiwiri chathela pomwepo. Osaonetsa kutopa komanso osafowoka, Williams Gondwa, Danger Left Winger wapitaaaa!
— ADD YOURS 👇😸
08/06/2026
Adah Bwana Micium M'hone watiuza kuti timuchenjeze coach wa Bullets akubwelayi kuti kuno kuli Ma Eagle.
“Muuzeni kuti kuri Blue Eagles FC, mzake Pasuwa akudziwa kale za team imeneyi”
___________________________
Like and follow Mpira Online
08/06/2026
Apule a FCB Nyasa Big Bullets anachita kuvaya okha Ku Lusaka Zambia kokatenga coach. With one mission; Adzazepule matimu.
07/06/2026
FRIENDLY MATCH RESULTS
Nsanje Medicals 0-6 Mighty Wanderers
Dedza Dynamos 1-2 Chimbiya Stars
07/06/2026
90+3'| ZEPU ZEPU ZEEEEEEEEPUUUUU ⚽
Kaliati scores making it 6-0
NSANJE MEDICALS 0-6 MIGHTY WANDERERS
— Matimu ang'ono ang'ono musamawapheeee, you Don't have to kill the younger teams!